Tuesday, January 24, 2012

Kamwazi (Typhoid Fever)

Typhoid fever (kamwazi) ndi matenda omwe a Malawi ambiri akuwadziwa. Matendawa, omwe nthawi zina anthu amasokoneza ndi malungo chifukwa chofanana zizindikiro, timayambitsa ndi tizirombo totchedwa bakiteria.
Matenda a kamwazi amayambitsa kutsegula m’mimba ndi ziwengo, kamba ka mtundu wa bakiteria womwe umayambitsa matendawa wa Salmonella typhi (S. typhi).
Nanga matendawa amayamba bwanji ndipo tingawapewe bwanji?
 Ka chilombo ka S. typhi  kamafala kudzela mu zakudya, zakumwa komanso madzi amene mwapezeka tizilomboti. Ngati mwadya kapena kumwa madzi omwe muli tizilombo toyambitsa kamwazi, tizilomboti timalowa mthupi mwanu kudzera mu matumbo. Kenako tizilomboti timachoka mu matumbo ndikulowa mu magazi momwe timafala ku ziwalo zosiyana siyana.
Kuopsya kwa matendawa ndi koti anthu ena amatha kukhala ndi matendawa mthupi mwao koma osadwala. Anthu oterewa amatchewa “afalitsi” (pa chizungu amati ma carriers), anthuwa amanka na falitsa matendawa asakudziwa. Anthuwa amafalitsa matendawa kudzera mu chimbudzi chawo, ndipo akhoza kufalitsa matendawa kwa zaka zambiri.
Zizindikiro za matendawa
Chizikiro choyamba ndi kutentha kwa mthupi, kuphwanya mthupi ndi kupweteka kwa m’mimba, ndi kutegula m’mimba.
Anthu ena amakhala ndi ziwengo zomwe zimaoneka ngati madontho ofira pa mimba ndi pa chifuwa.
Matendawa ndi oopsya choncho ndi chofunikira kuti ngati mwaona zizindikilozi, mupite ku chitala mwa msanga kuti mukalandire chithandizo.
Musayiwale kuti kamwazi ndi nthenda ya chisanu ndi chinayi (9) yoopsa pa dziko lonse lapansi pa matenda opatsirana.

No comments:

Post a Comment