Tuesday, January 17, 2012

Kodi Mukudziwa?

Sabata lapitali takhala tikukambirana za matenda opatsirana ndipo ndinaperkapo ndondomeko ya matenda khumi opatsirana omwe ali oopsya kwambiri pa dziko lapansi.

Lero tikambepo za nthenda yomwe ili ya chi khumi pa matenda oopsya kwambiri opatsirana pa dziko lapansi. Nthendayitu ndi ya nthomba yomwe pa chizungu imatchedwa smallpox.
Aliyense amane anabadwa kuyambira zaka za mbuyomo kulekezera 1978 wa chi Malawi ali ndi chipsyera chokhala ngati dzuwa pa mkono wao wa kumanja. Anthu ena nkumadabwa kuti kodi chipsyera chimenechi chinachokera kuti?
Chipsyerachitu ndi cha katemera wa matenda aja a nthomba omwe pa chizungu amatchedwa. Nthomba ndi imodzi mwa matenda oopsya kwambiri opatsirana pa dziko lapannsi. Nthendayi ili pa nambala 10 pa nthenda zoopsya kwambiri zopatsirana.  Ngakhale nthendayi inatha mumaiko ambiri, adakalipo maiko angapo omwe katemerayu adakaperekedwabe.
Nthendayi  imayambitsa ndi vairasi yotchedwa variola. Pachimake pa nthendayi mwa anthu zana limodzi (100) opezeka ndi matendawa anthu ochepera khumu okha ndi omwe amatha ku chira ku nthendayi.
Nkhani yosangalatsa ndi yakuti nthenda ya nthomba inagonjetsedwa ndipo inatha padziko lonse. Munthu omaliza kupezeka ndi matendawa adapezeka mu mwezi wa okotobala mu chaka cha 1977.
Tizilombo toyambitsa matendawa timabisala mu misempha ya khungu komanso mkamwa ndi pakhosi.  Momwe ti mapangitsa matuza omwe amadzala amaonekera kumanso komanso thupi lonse. Munthu akachira ku matendawa amakhala ndi zipsyera kumaso ndi mthupi, ena amachitika khungu kamba ka tizilomboti kupezeka mmaso, ena amapuwala ziwalo zosiyana siyana.
Mu chaka cha 1979 bungwe la World Health Organization (WHO) linalengeza kugonjetsa kwa matendawa.

No comments:

Post a Comment