Thursday, February 2, 2012

Influenza (Chimfine)

Influenza yomwe imadziwika kwambiri ndi dzina loti flu ndi matenda omwe amagwira mbalame komanso anthu. Matendawa anagwedeza dziko lonse mu chaka cha 2009 pamene kunagwa mlili wa chimfine cha mbalame(bird flu). Chimfine cha mbalame chinaopsya zedi chifukwa mbalame zodwala chimfinechi zi mapatsira anthu. Anthu omwe anatenga chimfinechi anadwala kwambiri ndipo ena anamwalira kumene.

Tsopano tisasokoneze influenza ndi matenda a chimfine omwe timadwala nthawi ndi nthawi omwe pa chizungu amati common cold ndipo ine ndi watcha chimfine cha wamba. Chimfine cha wamba chi ndi chija timakhala tikuyetsemula komanso kukha mamina. Chimfinechi chimatifoola ndipo chilakolako cha chakudya chimatheratu.  Chimfinechi timatha kudwala nthawi ina iliyonse koma chimachhuluka nyengo ya mvula ndi yozizira.

Tsopano kubwerera ku mutu wa lero, influenza  imasiyana ndi chimfine cha wamba  chifukwa influenza ndiyoopsya ndipo ikhoza kupha wodwalayo ngati salandira chithandizo.

 Zizindikiro

Zizindikiro za influenza zimafananira ndi zizindikiro za chimfine cha wamba. Munthu wodwala influenza amamva mpepo, kupweteka kokhala ngati kupalapala kwa pakhosi,    kupweteka kwa minyewa, kupweteka kwa mutu, chifuwa, ndi kufooka.

Kufala kwa matendawa

Matendawa amafala kudzera mu mpweya pamene munthu ayetsemula kapena kutsokomola. Influenza yo chokera kwa mbalame imafala kudzera mu zitosi komanso kudzera mu mamina a mbalame zomwe zikudwala matendawa. Munthu akhozanso kutenga matendawa pogwira malo omwe pagwera mamina, monga zitseko, pa tebulo ndi zina zotero.

Kupewa

·       Njira yoyambilira yozitetezera ku influenza ndi kulandira katemera yemwe amakonzedwa chaka chili chonse kulingana ndi mtundu wa chimfine omwe wavuta nthawi imeneyi.

·       Tikhoza kupewanso matendawa potseka pakamwa ndi mphuno ndi ka nsalu kominira pomwe tiyetsemula kuti tipewe kufalitsa tizilombo tofalitsa matendawa mu mpweya.

·       Nthawi zonse pewani kugwira m'maso, mphuno ndi pa kamwa, chifukwa tizilombo toyambitsa matendawa timatha kulowa mthupi kudzera njira imeneyi.

·       Ngati mwadwala influenza kapena chimfine cha wamba, khalani kunyumba ma ola 24 (24hrs) kuyambira nthawi yomwe kutentha kwa mthupi kwasiya.

Munthu wodwala influenza amatha kuchira mu sabata imodzi kapena awiri chiyambireni kudwala matendawa, koma ana ndi anthu achikulire, komanso omwe ali ndi matenda ena chimfinechi chikhoza kusokoneza mthupi ndi kuyambitsa chibayo kapena imfa.

Influenza ndi nthenda ya chisanu ndi chitatu (8) yopatsirana yoopsya kwambiri pa dziko lonse.

No comments:

Post a Comment