Thursday, January 12, 2012

Kupewa Matenda Opatsirana

Matenda opatsirana ndi matenda ena, ndi gwero la imfa zambiri, kulumala, komanso umphawi kwa zikwi zikwi za anthu pa dziko lapansi.


Ngakhale njira zilipo zopewera matendawa, komanso kupezeka kwa mankhwala osiyana siyana ochiza ena mwa matendawa, vutoli lidakalipobe.
Chifukwa chain vutoli la matendawa lidakalipobe?

Yankho kapena nditi mayankho alipo angapo, ena mwa iwo ndi awa;


    1. Anthu ambiri sadziwa kuti matendawa tikhoza ku wapewa


2. Anthu ambiri sakudziwa njira zopewera matendawa


3. Kusowa kwa mankhwala omwe amathandiza ku chepetsa komanso kuchiza matendawa


4. Kuchepa kwa maphunziro, choncho anthu ambiri satha kuwerenga ndi kulemba ndipo sangathe kuwerenga za njira zopewera kapena kupeza chithandizo ku matendawa.


5. Ku kwera mtengo kwa mankhwala komanso zipatala zolipira komwe anthu angathe kupeza ena mwa mankhwala oti angawathandize ku matendawa


6. Umphawi womwe umapangitsa anthu kukhala m’malo komanso kumwa madzi ndi kudya zakudya zoti si za ukhondo


Nanga tingathandizane bwanji kuti tichepetse kapena kupewa kumene matenda opatsiranawa?

Chifukwa cha kuopsya kwa matenda opatsirana, maiko osiyana siyana pa dziko lonse anagwirizana pa mfundo yotchedwa “Millenium Development goals” omwe pa Chichewa tinganti “Mfundo za chitukuko muchilimika cha mileniyamu”. Imodzi mwa mfundo zomwe anagwirizana ndi :


Kuthetsa komanso kutembenuza njira za kufala kwa matenda opatsirana pofika chaka cha 2015.


Kodi maiko wa akwaniritsa bwanji mfundo imeneyi?

Ilitu ndi funso lomwe dziko lili lonse liyenera kuyankha. Maiko osiyana siyana akonza njira zomwe akutsata kuti athane ndi vuto la matenda opatsiranawa. Zina mwa njirazi ndi;


1) Kuonetsetsa kuti anthu aphunzitsidwe njira zopewera matenda opatsirana


2) Kuonetsetsa kuti anthu akulandira mankhwala oyenerera ochepetsa komanso ku chiza matendawa


3) Kuonesetsa kuti anthu ali ndi madzi a ukhondo komanso akuphunzitsidwa njira zosiyana siyana za ukhondo.


Chikhazikitsileni mfundo za chitukukuko mu chilimika cha mileniyamu mu chaka cha 2000, zina mwa zinthu zomwe maiko akwaniritsa ndi;


· Kuchepetsa kwa imfa chifukwa cha matenda a chikuku ndi pafupi fupi 92% mu Africa ndi Madera a ku mvuma kwa Nyanja ya Mediterenian (East Medeterenian)

· Kukwaniritsa ku chiza matenda a TB mu Madera ambiri a ku Mwera cha ku mvuma kwa Asia (South East Asia)


· Pafupifupi kuthetsa matenda a Polio ndi matenda ena opatsirana kudzera mu tinyongolotsi (worm diseases)

Izi ndi zina mwazitsanzo za njira zomwe maiko akuyesetsa kukhazikitsa mu kulimbana ndi matenda opatsirana.









No comments:

Post a Comment